Top Latest News & Reports

NDINE WOKHUTIRA
13 Jan 2025

NDINE WOKHUTIRA

Wachiwiri kwa Kazembe wa Dziko la Britain kuno ku Malawi a Olympia Wereko-Brobby wati ndi wokhutira ndi mmene Boma la Malawi kudzera ku Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi (DoDMA) ndi abwenzi ake akulimbikitsira ntchito zochilimika ku ngozi zogwa mwadzidzidzi.

Iwo anena izi Lachitatu (pa 8 January, 2025) ku Nsanje pomwe motsogozana ndi akuluakulu a boma la America komanso DoDMA, anakayendera maanja pafupifupi 2,000 omwe anasamuka m’dera la Makhanga (lomwe limakhudzidwa kwambiri ndi kusefukira kwa madzi) kwa TA Mlolo n’kukakhala kwa TA Mbenje, m’boma la Nsanje lomwelo.

“Ndili okhutira ndi zomwe ndaona ndipo Boma la Britain lipitiriza kuthandiza dziko la Malawi pa ntchito yochilimika ku ngozi zogwa mwadzidzidzi. Ndilinso okondwa ndi momwe anthu osamukawa achilimikira ngakhale akukumana ndi mavuto osiyanasiyana,” anatero a Wereko-Brobby.

Mwa zina, DoDMA inakumba mijingo ku dera latsopanoko komanso kulambula misewu pomwe bungwe la Give Directly linapereka ndalama za pakati pa K300,000 mpaka K1.2 miliyoni kwa maanja kuti zithandizire pa ntchito yomanga nyumba zawo.

A Wereko-Brobby, anakayenderanso Bangula Humanitarian Staging Area, omwe ndi malo olumikizitsa ntchito zokonzekera ku ngozi zogwa mwadzidzidzi. Mwa zina, malowa amasungira chakudya, mafuta a galimoto komanso zipangizo zopulumutsira anthu pa ngozi monga mabwato.

 

Visitors Counter

1032096
Today
Yesterday
This Week
Last Week
This Month
Last Month
All days
469
1645
4722
1020089
16053
22737
1032096

Your IP: 18.226.187.60
2025-01-15 08:30