Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa Dziko Lino Dr. Michael Usi anakayendera ntchito yopereka thandizo kwa maanja okhudzidwa ndi njala m'maboma a Chikwawa ndi Thyolo.
Akuluakuluwa saadalekere pompo koma kukhotanso ku Kampu ya Nyamithuthu, yomwe ikusunga maanja pafupifupi 2,000 omwe adathawa zipolowe m’dziko la Mozambique. Uku anacheza ndi anthu akuluakulu komanso ana (omwe anawapeza akusewera mpira ndi masewero osiyanasiyana), kumva za mmene akukhalira komanso mavuto omwe akukumana nawo.
Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa Dziko Lino Dr. Michael Usi Lachisanu (pa 27 December) anakayendera ntchito yopereka thandizo kwa maanja okhudzidwa ndi njala m'maboma a Chikwawa ndi Thyolo.
Pa ulendowu, a Usi anayankhulana ndi ena mwa okhudzidwa za mmene ntchitoyi ikuyendera.
Iwo anathandizanso kunyamulira matumba a chimanga anthu okhudzidwa, kuphatikizapo achikulire.
AYENDERA NTCHITO YOKONZEKELA KUBWEZELETSA MIYOYO YA ANTHU OHUDZIKA KU NGOZI ZOGWA MWADZIDZIDZI
Motsogozedwa ndi Mkulu wa Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi M’busa Charles Kalemba, akuluakulu ochokera ku ofesi za a Kazembe a maiko a Britain komanso United States kuno ku Malawi Lachinayi (pa 9 January, 2025) anakayendera ntchito zokonzekera, kubwezeretsa miyoyo ya anthu okhudzidwa komanso kuchilimika ku ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Mwa zina, iwo anakayendera sikimu ya ulimi wa nthilira ya Chimwalambango, yomwe idamangidwa ku Nsanje ngati njira imodzi yobwezeretsera m’chimake miyoyo ya anthu omwe adakhudzidwa ndi Namondwe wa Idai.
Akuluakuluwa, omwe ndi kuphatikizapo Wachiwiri kwa Kazembe wa Boma la Britain kuno ku Malawi a Olympia Wereko-Brobby, Woyang’anira Ntchito mu Ofesi ya Kazembe wa Boma la America kuno ku Malawi a Pamela Fessenden anakaonanso mmene othandiza kupulumutsa anthu pa nthawi ya ngozi amagwilira ntchito yawo mu mtsinje wa Shire.
Iwo anafikanso kwa TA Mbenje komwe anakambirana ndi ma volunteer komanso komiti (yoona za ngozi zadzidzidzi) pa za ntchito zomwe akugwira motsogozedwa ndi mothandizana ndi Bungwe la Malawi Red Cross Society - MRCS.
Akuluakuluwa saadalekere pompo koma kukhotanso ku Kampu ya Nyamithuthu, yomwe ikusunga maanja pafupifupi 2,000 omwe adathawa zipolowe m’dziko la Mozambique. Uku anacheza ndi anthu akuluakulu komanso ana (omwe anawapeza akusewera mpira ndi masewero osiyanasiyana), kumva za mmene akukhalira komanso mavuto omwe akukumana nawo.
AN UPDATE ON CYCLONE DIKELEDI
NDINE WOKHUTIRA
Wachiwiri kwa Kazembe wa Dziko la Britain kuno ku Malawi a Olympia Wereko-Brobby wati ndi wokhutira ndi mmene Boma la Malawi kudzera ku Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi (DoDMA) ndi abwenzi ake akulimbikitsira ntchito zochilimika ku ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Iwo anena izi Lachitatu (pa 8 January, 2025) ku Nsanje pomwe motsogozana ndi akuluakulu a boma la America komanso DoDMA, anakayendera maanja pafupifupi 2,000 omwe anasamuka m’dera la Makhanga (lomwe limakhudzidwa kwambiri ndi kusefukira kwa madzi) kwa TA Mlolo n’kukakhala kwa TA Mbenje, m’boma la Nsanje lomwelo.
“Ndili okhutira ndi zomwe ndaona ndipo Boma la Britain lipitiriza kuthandiza dziko la Malawi pa ntchito yochilimika ku ngozi zogwa mwadzidzidzi. Ndilinso okondwa ndi momwe anthu osamukawa achilimikira ngakhale akukumana ndi mavuto osiyanasiyana,” anatero a Wereko-Brobby.
Mwa zina, DoDMA inakumba mijingo ku dera latsopanoko komanso kulambula misewu pomwe bungwe la Give Directly linapereka ndalama za pakati pa K300,000 mpaka K1.2 miliyoni kwa maanja kuti zithandizire pa ntchito yomanga nyumba zawo.
A Wereko-Brobby, anakayenderanso Bangula Humanitarian Staging Area, omwe ndi malo olumikizitsa ntchito zokonzekera ku ngozi zogwa mwadzidzidzi. Mwa zina, malowa amasungira chakudya, mafuta a galimoto komanso zipangizo zopulumutsira anthu pa ngozi monga mabwato.