Motsogozedwa ndi Mkulu wa Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi M’busa Charles Kalemba, akuluakulu ochokera ku ofesi za a Kazembe a maiko a Britain komanso United States kuno ku Malawi Lachinayi (pa 9 January, 2025) anakayendera ntchito zokonzekera, kubwezeretsa miyoyo ya anthu okhudzidwa komanso kuchilimika ku ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Mwa zina, iwo anakayendera sikimu ya ulimi wa nthilira ya Chimwalambango, yomwe idamangidwa ku Nsanje ngati njira imodzi yobwezeretsera m’chimake miyoyo ya anthu omwe adakhudzidwa ndi Namondwe wa Idai.
Akuluakuluwa, omwe ndi kuphatikizapo Wachiwiri kwa Kazembe wa Boma la Britain kuno ku Malawi a Olympia Wereko-Brobby, Woyang’anira Ntchito mu Ofesi ya Kazembe wa Boma la America kuno ku Malawi a Pamela Fessenden anakaonanso mmene othandiza kupulumutsa anthu pa nthawi ya ngozi amagwilira ntchito yawo mu mtsinje wa Shire.
Iwo anafikanso kwa TA Mbenje komwe anakambirana ndi ma volunteer komanso komiti (yoona za ngozi zadzidzidzi) pa za ntchito zomwe akugwira motsogozedwa ndi mothandizana ndi Bungwe la Malawi Red Cross Society - MRCS.
Akuluakuluwa saadalekere pompo koma kukhotanso ku Kampu ya Nyamithuthu, yomwe ikusunga maanja pafupifupi 2,000 omwe adathawa zipolowe m’dziko la Mozambique. Uku anacheza ndi anthu akuluakulu komanso ana (omwe anawapeza akusewera mpira ndi masewero osiyanasiyana), kumva za mmene akukhalira komanso mavuto omwe akukumana nawo.