Update on cyclone FAIDA
KWANU N'KWANU
...Boma la Mozambique Lapempha Mzika Zake Kuti Zibwelere Kwawo.
Boma la Mozambique lapempha mzika zake zomwe zidathawa zipolowe zokhudza chisankho ndipo zikukhala m'dziko muno kuti zibwelere kwawo.
Mtsogoleri wa Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi Mai Luisa Celma Meque apereka pempholi Lachisanu (pa 31 January) pa kampu ya Nyamithuthu m'boma la Nsanje pomwe anakayendera zina mwa mzika zoposa 7,000 zomwe zili pa kampuyi.
"Sichapafupi kuti dziko lidzisamalira mzika za dziko lina mwachikondi ngati mmene ziliri kuno. Mmalo mwa President Chapo, ndikuthokoza mmene Boma la Malawi linakulandilirani komanso mmene likukusamalirani. Izi zikusonyeza ubale wabwino pakati pa maiko athu.
"Ngakhale izi zili chonchi, dziwani kuti zipolowe zinatha m'dziko lathu ndipo muli bata. Tiyeni tibwelere kwathu," anatero a Meque uku anthu akufuula mokondwera.
Mai Meque, omwe anafika m'dziko muno dzulo kudzera ku chipata cha Mwanza pa mdipiti omwe panalinso galimoto zikuluzikulu zitatu zomwe zinanyamula katundu monga mpunga, mchere, ufa ndi mabulangete, ati akabwelera kwawo akakonza ndondomeko yoti anthuwo abwelere kwawo.
Padakali pano, a Meque ndi mdipiti wawo abwelera ku Mozambique kudzera pa chipata cha Mwanza.