Boma kudzera ku Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi (DoDMA) mogwirizana ndi mabungwe osiyanasiyana likupereka thandizo la chakudya kwa anthu 5.7 miliyoni okhudzidwa ndi njala pansi pa ndondomeko ya 2024-25 Lean Season Response.
Ntchitoyi idayamba mu September chaka chino ndipo ikuyembekezeka kutha m'mwezi wa February/March 2025.
Izi ndi zina mwa zithunzi zoonetsa ntchito yopereka thandizoli m'makhonsolo.
Ojambula: Ogwira ntchito m'makhonsolo.