Top Latest News & Reports

BWENZI LENILENI LIMAWONEKA PAMAVUTO
18 Nov 2024

BWENZI LENILENI LIMAWONEKA PAMAVUTO

…Ofesi Ya Kazembe wa Dziko la China Lapereka Matumba a Ufa 1,320 Kwa Maanja Okhudzidwa ndi Njala

Ofesi ya Kazembe wa Dziko la China kuno ku Malawi Lachinayi (pa 7 November, 2024) lapereka matumba a ufa 1,320 [lililonse lolemera makilogalamu 25] a ndalama zokwana K42.8 miliyoni ku maanja omwe akhudzidwa ndi njala mmudzi mwa Sonkhwe, m’dera la Mfumu Yaikulu Kalumbu m’boma la Lilongwe.

Poyankhula pomwe amalandira thandizoli mmalo mwa Boma la Malawi, Mlembi wamkulu ku Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi M’busa Charles Kalemba anati thandizoli lawonetseratu kuti dziko la China ndi limodzi mwa abwenzi enieni a dziko la Malawi.

“Bwenzi lenileni siliwoneka pachisangalaro pokha, koma pamavuto. Thandizoli ladza pomwe Boma la China posachedwapa lapereka matumba 36,600 a mpunga kuti athandize pa ntchito yofikira anthu 5.7 miliyoni okhudzidwa ndi njala. Tikulumikizananso ndi China mwakuya kuti tilimbikitse ntchito za ulimi wa nthilira ndikuphwanya goli la njala. Ngati dziko, tikuyenera kuchitapo kanthu, sitingamangolandira chithandizo, tikuyenera kukhala odzidalira pa chakudya chifukwa zonse zodziyenereza kutero monga nyanja ndi mitsinje tili nazo,” anatero a Kalemba.

Mmawu ake, mmodzi mwa akuluakulu ku Ofesi ya Kazembe wa dziko la China kuno ku Malawi a Wang Hao anati saakanamangoyang’ana anzawo akufunika thandizo.

“Ifenso ndiwokhudzidwa ndipo tikumva nawo kuwawa polingalira za vuto la njala lomwe lakhudza dziko la Malawi. N’chifukwa chake taikapo mtima kuthandiza ndi kangachepe. Tionetsetsanso kuti tikugwira ntchito limodzi kuti tipititse patsogolo miyoyo ya anthu a maiko awiriwa,” anatero a Hao.

 

Visitors Counter

980581
Today
Yesterday
This Week
Last Week
This Month
Last Month
All days
401
1929
7252
958701
35274
136143
980581

Your IP: 18.119.105.155
2024-11-21 07:34