…Boma La India Lapereka Matumba 22,000 a Mpunga; Othandizira Okhudzidwa ndi Njala
Boma la India lapereka ma tani 1,100 (omwe ndi matumba 22,000 olemera makilogilamu 50 lililonse) a mpunga ku Boma la Malawi kuti athandizire pa ntchito yofikira anthu omwe ali pachiopsezo cha njala.
Poyankhula Lachitatu ku Kanengo mu Mzinda wa Lilongwe pa mwambo wopereka mpungawu, Kazembe wa Boma la India ku Malawi Shri S. Gopalakrishnan anati ubale wa maiko a India ndi Malawi si wa lero kotero saakanangoyang’ana kumbali pomwe mzika zake zikufunika thandizo.
“Ubale wa anthu a maiko awiriwa unayamba zaka 140 zapitazo pomwe ubale wa ukazembe unayamba mu 1964. Nde titamva kuti mtsogoleri wa dziko lino [ Dr Lazarus Chakwera ] walengeza kuti dziko lino ndi malo a ngozi ndipo likufunika thandizo, tinachiwona chanzeru kuti tithandize achimwene ndi achemwali athu omwe akukhudzidwa ndi vuto la njala,” anatero a Gopalakrishnan.
Mmau ake, Mlembi Wamkulu ku Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi M’busa Charles Kalemba anathokoza boma la India mmalo mwa Boma la Malawi chifukwa cha thandizoli.
“Mpunga wonse wafika ndipo tayamba kale kugawa kwa anthu okhudzidwa. Tayambanso kugawa chimanga ndi thandizo lina m’maboma omwe akuyenera kulandira thandizo kwa miyezi isanu [5], inayi [4] komanso itatu pansi pa ndondomeko ya 2024/25 lean season response," anatero a Kalemba.