Boma kudzera ku Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi (DoDMA) Lachitatu (pa 18 September) lakhazikitsa ntchito yopereka thandizo la chakudya kwa anthu 5.7 milliyoni pansi pa ndondomeko ya 2024-25 Lean Season Response.
Izi zadza pomwe Komiti ya Malawi Vulnerability Assessment, yomwe imapanga kawuniwuni wa mmene dziko lino likhalire ndi chakudya, idalengeza mmiyezi yapitayi kuti anthuwa adzafunika thandizo la chakudya kuyambira m’mwezi wa October chaka chino mpaka wa March chaka cha mawa.
Koma poyankhula pomwe amakhazikitsa ntchitoyi mu Mzinda wa Blantyre, Mkulu Woona Zokonzekera Ngozi Zadzidzidzi ndi Kuthandiza Okhudzidwa M’busa Moses Owen Chimphepo anati boma linawunikira kuti vuto la njala lakula kwambiri m’dziko muno chifukwa anthu saanakolore mokwanira kutsatira nyengo ya El Nino yomwe inadza ndi ng’amba komanso kusefukira kwa madzi.
“Sitingadikire [kuyamba kupereka thandizo] mpaka October, n’chifukwa chake tayambiratu panopa; komanso kuyambira mu July chaka chino mpaka August, takhala tikupereka ufa ndi chimanga zoposa matumba 30,000 m’maboma asanu ndi anayi omwe tinalandira ma lipoti a njala yoopsa. Ngati boma, tionetsetsa kuti tafikira onse okhudzidwa ndi njala ndipo tikupempha ma khonsolo ndi makomiti a m’madera kuti aonetsetse kuti okhawo ovutikitsitsa ndi omwe akulandira thandizoli,” anatero M’busa Chimphepo.
M’mau awo, Mkulu Woyendetsa Ntchito za Khonsolo ya Mzinda wa Blantyre a Lytton Nkata anathokoza boma chifukwa cha machawi poyambitsa ntchito yopereka thandizo kwa okhudzidwa.