Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi (DoDMA) ikudziwitsa anthu onse m’dziko muno kuti kutsatira ma lipoti ochokera ku Nthambi Yoona Za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo, pali chiyembekezo choti mvula yamphamvu igwa mmaboma a Chikwawa ndi Nsanje komanso mmadera a mmbali mwa nyanja zomwe zitha kudzetsa ngozi ya madzi osefukira kuyambira pa 21 mpaka pa 22 December, 2022. Mvulayi ikuyembekezeka kudza ndi mphepo yamkuntho komanso mphenzi.
Pachifukwachi, Nthambiyi ikupempha kuti titsatire malangizo awa kuti tichepetse chiopsezo chokhudzidwa ndi ngozizi:
Tisazengereze, tisakakamire, tiyeni tisamukire mmadera a kumtunda.
Tipewe kuoloka mitsinje yosefukira komanso kuyenda mmadera omwe madzi asefukira.
Ngati palibe njira ina ndipo tikuyenera kuyenda mmadzi kuti titeteze moyo, tiyende mmalo omwe madzi sakuthamanga. Tigwiritse ntchito muyezo kuti tidziwe za kuya kwa malo omwe tikuponda.
Tisayandikire mawaya a magetsi, dziwitsani msanga a ESCOM, amfumu kapena a polisi za mawaya kapena mapolo a magetsi omwe agwa.
Tisathamangire kupulumutsa katundu yemwe akukokoloka ndi madzi, tionetsetse kuti moyo wathu ndi wa ena ngotetezeka.
Tikhale tcheru pomwe mphepo yamkuntho ikuomba, denga ndi zidutswa zitha kutivulaza ngakhalenso kutipha kumene.
Tisakhale moyandikana ndi zitseko komanso mawindo pomwe mphepo yamkuntho ikuomba.
Ngati tikuyendetsa galimoto, tisathamangitse. Tionetsetse kuti mazenera a galimoto yathu ndiwotseka.
Tisabisale pansi pamtengo pamene mvula ikugwa. Izi zimadzetsa chiopsezo chowombedwa ndi mphenzi.
Ngati tingakwanitse, tipereke thandizo loyambilira (first aid) kwa ovulala ndipo tipite nawo kuchipatala mwansanga.
Tionere, kumvera komanso kuwerenga uthenga wa za nyengo kuti tidziwe momwe nyengo ikhalire mdera lathu.
Padakali pano, DoDMA ikuyang’ana mwatcheru za chenjezoli ndipo yadziwitsa kale nthambi zothandiza kupulumutsa anthu pangozi monga Malawi Defence, Malawi Police ndi Marine Department kuti zikhale zokonzeka kukagwira ntchito mmadera omwe ali pachiopsezo chokhudzidwa ndi ngozi ya madzi osefukirayi.
DoDMA ikulengezanso mauthenga a pawailesi omwe akulunjika za mmene anthu angapewere komanso kuchepetsa chiopsezo chokhudzidwa ndi Ngozi za madzi osefukira, mphenzi komanso mphepo yamkuntho.
Ngati mukufuna kudziwa zambiri za izi, imbirani mneneri wa Nthambi Yoona Za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi a Chipiliro Khamula pa 0999 043 228 kapena 0884 572 844.
22 December, 2022.
Charles Kalemba
COMMISSIONER FOR DISASTER MANAGEMENT AFFAIRS
Disaster Risk Reduction is Everyone’s Responsibility!